Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 91
Miyambi ya Patsokwe
popeza zamawa sizidziwika, ndi nzeru kumasunga zoti zidza-
tithandize pamavuto.
Kufuna Lumbe chifukwa cha mthenga, koma osadya nyama
yake.
-Anthu ena amakukonda chifukwa cha zabwino zimene uli
nazo, zikatha amakuthawa.
Kufunsa ndi kudziwa njira.
-Ngati sukudziwa zinazake, m’malo mongozichita, ndi bwino
kufunsa kaye kuti uzichite bwino.
Kugona m’kuka n’chitatu.
-Mwambiwu umanena kuti kugona m’kuka, kapena kuti nyum-
ba ya mayi ako, ndi uchitsiru wotheratu. Munthu akakula ama-
funika kudziimira payekha. Choncho, si bwino kumadalira ma-
kolo nthawi zonse kuti atithandize.
Kugona pakati n’kuyambirira.
-Kuti munthu upeze malo abwino pagulu, kaya ukukagona ku-
maliro, umayenera kufulumira kwambiri. Ndi bwino kumachita
zinthu moyambirira ngati ukufuna zikuyendere bwino. Pofuna
kuchita zinthu ndi bwino kuzichita mosachedwa.
Kugonagona kumapangitsa tsitsi kufula.
-Mawuwa amatanthauza kuti kukhala ndi moyo, kapena kuti
kugona masiku ambiri, kumachititsa tsitsi liyere kapena kuti
ukalambe. Akuluakulu ndi amene amadziwa bwino zapadzikoli.
Choncho, ndi bwino kumawafunsa malangizo pa nkhani zosi-
yanasiyana.
Kuika mkute n’kupangana.
-Munthu akamachita zinthu ndi ena, ndi bwino kumayamba
mwapangana, osamangochita zokomera munthu mmodzi.
90