Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Página 89

Miyambi ya Patsokwe Kudya n’kudyabe, kumbuka uko unachokera. -Tikakhala pabwino tisamaiwale kumbuyo, tizikumbukira ma- kolo, achibale komanso aphunzitsi omwe anatithadiza. Kudya n’kuika. -Aliyense ayenera kudya zimene wapeza. Kudya n’kunyambitira komanso kunyong’olera. -Si kulakwa kusonyeza poyera kuti wakhutitsidwa ndi zimene wachita kapena wapatsidwa. Kudya pawiri kunang’ambitsa fisi miyendo. -Tizichita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi. Kudya za m’gomo yankhwangwa, za m’khasu osadzidya. -Tiyenera kukhala anthu okhulupirika, osunga chinsinsi. Pali zinthu zina zomwe sitingaime pachulu n’kumanena. Kudyerana masuku pamutu. -Mawuwa amanena za kuchenjeretsana. Anganenedwenso ngati wina akuchitira zake zopanda chilungamo pomuchenjeretsa. Timanena kuti, “Akumudyera mnzake masuku pamutu.” Kudza kwa mafinya ndi minga pomweponso. -Mawuwa amanenedwa anthu akagwira wakuba limodzi ndi katundu amene waba. Kudzikuza kwa Udzudzu kouza Njovu kuti ukupanga mdidi. Kudzikuza si kwabwino. Udzudzu wina unali pakhutu pa njovu. Njovu imaoloka mulatho, ndiye imati ikamayenda, mu- lathowo unkangoti teketeke. ndiye kaudzudzu kaja kananena kuti, ‘Koma ndiye tikutekesa mulathotu!’ Kufa saferana. -Pali zinthu zina zomwe aliyense amafunika kuchita yekha ko- manso kusankha yekha chifukwa zotsatira za zimene wasankhazo adzakumana nazo yekha. 88