Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 88
Miyambi ya Patsokwe
Kudandaula sikuthetsa m’landu koma kuyankhulapo.
-M’malo momangodandaula ndi bwino kuchita khama kuti vuto
lathulo lithe.
Kudandaula sikuthetsa njala koma kusunja.
-M’malo momangodandaula ndi bwino kuchita khama kuti vuto
lathulo lithe. Kusunja ndi kupempha kwa ena kuti akuthandize.
Kudumpha dzenje n’kulionera patali.
-Ukadziwa vuto ukhoza kupeza njira yolipewera.
Kudya kudamanitsa vimvi mapiko.
-Tisamachedwe kuchita zinthu zimene zingadzatithandize
m’tsogolo. Vimvi inachedwa kupita kokalandira mapito chifu-
kwa cha kudya. Pamene imapitako inapeza mapiko atatha.
Kudya kwa mnzako sungamwere madzi.
-Munthu azidzidalira yekha pogwira ntchito m’malo modalira
ena. Sungamawerengere kuti chifukwa choti wina wadya ndiye
kuti iwe umwera madzi, madziwo akapeza chiyani m’mimbamo
popeza amadya ndi mnzako! Nafenso tisamadalire kuti ena ag-
wire ntchito kuti atithandize, tizichita khama.
Kudya lapi, kulima kwete.
-Pali anthu ena omwe amasangalala pakudya, koma akauzidwa
kuti agwire ntchito amakana kapena amanamizira kudwala.
Munthu amayenera kudya thukuta lake. Kuti munthu apeze
chinthu amayenera kuchivutikira. Ena kuwauza kuti, “Iwe tiye
kumunda,” amayankha kuti, “Ndikudwala ineeeeee!” Koma ku-
wauza kuti, “Tiye kumowa,” uwamva akuyankha kuti, “Bola
ndikhoza kudzikoka.”
Kudya n’kudya, umakumbuka polowa.
-Tikakhala pabwino tisamaiwale kumane tachokera kapena
mavuto omwe takhala tikukumana nawo.
87