Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 86

Miyambi ya Patsokwe Tisamangodikira kuti ena azitithandiza ifeyo n’kumangokhala phwi osawathandiza. Zikatero nawoso amatopa n’kusiya kutithandiza. Konza kapansi kuti kam’mwamba katsike. -Ngati ukufuna kulandira zabwino kuchokera kwa anthu enaake umayenera kuonetsa khalidwe labwino kuti anthuwo akopeke. Munthu ukafuna kuti anthu akuchitire chabwino, umafunika kuyamba ndiweyo kuwachitira zabwino. Kopanda ntchito umataya. -Chilichonse ndi chaphindu panthawi yake. Koyenda sawononga pakumwa. -Munthu ukakhala kwanu si bwino kumachitira alendo mwano. Kubala kwa chule ndi kwa thesi n’kumodzi. -Mawuwa amatanthauza kuti onse ndi anthu ngakhale atakhala kuti ndi osiyana khungu, chikhalidwe, msinkhu, kukongola ndi zina zotero. Kuchedwa kumphero mseche uchuluke. -Mawuwa amanenedwa akaona kuti azimayi akuchedwa kubwera kuchokera kumadzi kapena kuntchini. Amaona kuti kumeneko amachedwa ndi kunena miseche. Kuchenjera kwa Kalulu kunaphetsa Ankhwere. -Pali anthu ena odziwa kuzunguza lirime kwambiri, omwe amatha kuika anzawo m’mavuto ndi zonena zawo. Tiyenera ku- chenjera ndi anthu oterewa. Kuchenjera kwa Nkhandwe, kolangiza ena kuti adule michira chifukwa wake waduka. -Osamapusitsa ena n’cholinga choti nawonso agwere m’mavuto, kapena kuti mufanane. 85