Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 85
Miyambi ya Patsokwe
Khotekhote ngwa njoka, umatsata kwaloza mutu.
-Pofuna kumvetsa nkhani ndi bwino kupeza mutu wa nkhaniyo.
Khotekhote ngwanjira, palinga mtima mpomwepo.
-Ngakhale njira yopezera chinthu itakhala yaitali, ngati munthu
waikapo mtima umachipeza.
Khoza limapita ndi mwini dzanja.
-Sungakakamize munthu kuchita zimene sakufuna.
Khwangwala wamantha adafa ndi ukalamba.
-Munthu akasamalira moyo wake amakhala ndi moyo wautali.
Koma tambwali amafa nthawi yake isanakwane. Munthu
wamantha amakhala zaka zambiri ndi moyo chifukwa man-
thawo amamuthandiza kuti asamachite mphulupulu zomwe
zingachititse kuti afe msanga.
Kodi kuimirira kwakupindulitsa chiyani, anzako akupindula
ndi werawera?
-Tizigwira ntchito molimbika kuti tipeze zosowa zathu. Polima
timawerama osati kuimirira.
Kodi mtengo wopanda tsinde mudauona?
-Chilichonse chimakhala ndi poyambira pake.
Komekome ngwa m’kamwa, kampeni kali pafunkha.
-Pali anthu ena omwe amasangalala ndi anzawo pakamwa
pokha, koma mumtima mwawo muli chiwembu.
Komwe wachoka osamatsekako ndi mwala, koma mayani.
-Ndi bwino kumasiyana bwino ndi anthu ukamachoka
pamudzi, chifukwa tsiku lina udzabwererako.
Kondwerekondwere samatha, kumbuka zili kudza.
-Posangalala pamafunika kumaganizira zam’tsogolo.
Konsekonse mpeni wansengwa.
-Tiyenera kumachitirana zabwino kapena kumathandizana.
84