Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 84

Miyambi ya Patsokwe umachitira ndi chako. N’zofanana ndi kubwereka khasu la apongozi n’kumaona kuti silingakuthandize chifukwa lilibe chimbetete kapena kuti kachibonga koswera zigulumwa. Khasu limaposa amako ndi atate wako. -Munthu umayenera kumadzidalira pamoyo wako pogwira ntchito m’malo mokhala mlesi. Khasu lobwereka silichedwa kuthyoka. -Chobwereka suchedwa kuchita nacho ngozi. Khola ndi mathole. -Khola lodalilika silikhala ndi ng’ombe zikuluzikulu zokhazo- kha. Limafunika kukhala ndi ng’ombe zazing’ono zomwe zimatchedwa mathole. Ana ndi tsogolo la dziko. Khoswe akakhala pamkhate sapheka. -Kumakhala kovuta kuti uweruze mlandu wa m’bale wako mak- amaka akapezeka kuti iyeyo ndi amene ali wolakwa. Khoswe amaluma n’kuuzira. -Khoswe amati akaluma amauzira kuti munthu asamve kupweteka kwambiri. Tikamanena zinthu ndi bwino kumachita zinthu mozindikira kuti tisakhumudwitse ena. Mwachitsanzo, tikamapatsa ena malangizo, ndi bwino kumawapereka mwachikondi. Kumakhala ngati taluma n’kuuzira. Khoswe sagona ndi nyungu. -Nyungu ndi nthangala za mawungu zomwe ena amazigwiritsa ntchito ngati mtedza. Mwambiwu umatanthauza kuti zinthu zo- dana sizikhalira pamodzi. Komanso sungaike munthu wakuba pamalo omwe pali zinthu zomwe angabe. Khoswe wapatsindwi anaululitsa wapadzala. -Chinthu china chimatha kuululitsa chinthu china chomwe chi- nali chobisika. 83