Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 83
Miyambi ya Patsokwe
chake. Ndiye kachizindikiro kangachepe bwanji tizikhala nako
tcheru.
Kaulamchokero adaika phale padzuwa.
-Tikamafuna kuchoka pamalo kapena pamudzi, tisamachoke ti-
tawonongapo chifukwa mawa tidzafuna kubwererakonso.
Kaulere sikachepa.
-Tiyenera kumathokoza tikapatsidwa zinthu ngakhale zitakhala
zochepa.
Kawalewale adapweteka m’dayeretsa.
-Tizichenjera ndi zosangalatsa zomwe pamapeto pake zimabw-
eretsa mavuto.
Kawerewere kadautsa njovu.
-Ngati sitisamala, chinthu chaching’ono chitha kubutsa mavuto
aakulu monga mmene kamoto kakang’ono kamayatsira
nkhalango.
Kayenda m’sana kapenya malowo.
-Ngati pamlandu munthu akuyankhula m’maso muli gwa, ndiye
kuti ali ndi podalira.
Kayenda m’sana katamanda maoloko.
-Tizidalira abale ndi alongo athu chifukwa ndi amene amadza-
tigwira dzanja tikadzakumana ndi mavuto.
Khalidwe silifanana ndi kudziwika.
-Munthu akhoza kukhala wodziwika koma wopanda khalidwe.
Khama lidaphetsa mbewa zapachulu.
-Tikafuna kupeza chinthu tiyenera kuchita khama kwambiri.
Koma tikachita khamalo, tizidyerera thukuta lathu.
Khasu la apongozi lopanda chimbetete.
-Munthu sungagwiritse ntchito chinthu chobwereka m’mene
82