Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 82
Miyambi ya Patsokwe
Kapinji mayendayenda kasiya anzake asewera.
-Kuchenjeretsa kapena kuyendayenda popanda zifukwa zomve-
ka kumabweretsa mavuto.
Kaponda mvichili.
-Mawuwa akutanthauza mawu abodza ochokera kwa munthu
amene zokamba zake sizimakhala zoona.
Kapota nyanga, n’kulinga katachenjera.
-Ngati nyama yafika poyamba kupota nyanga ndiye kuti inali
yochenjera pothawa alenje ndipo imakhala ndi moyo wautali.
Munthu amene wafika pokalamba ndiye kuti anapewa zinthu
zambiri zomwe zikanatha kuwononga moyo wake.
Kapusa n’kamake, kopanda amake kachenjera.
-Anthu ambiri amene amakhala ndi makolo awo amapusa.
Amachenjera makolo awo akamwalira. Umasiye umaphunzitsa
zambiri.
Kasiyagoli.
-Mawuwa amanena za munthu yemwe amanena bodza
lotsekemera n’cholinga choti zinthu zimuyendere bwino. An-
ganenedwenso ponena za munthu amene wapulumuka pamlan-
du chifukwa chodziwa kuyankhula.
Kasule wa m’chikho cholimba kuwawa.
-Munthu amene amachita zoipa amakumana ndi mavuto oopsa
ngati mmene chikho cholimba chimatulutsira madzi kapena
mowa wowawa.
Kathabwalika thumba lamwala lokanika kusoka.
-Awa ndi mawu okokomeza onena za munthu waukamberem-
bere, tambwali.
Kati deru kaopsa mlenje.
-Kanthu sikachitika popanda chifukwa kapena choyambitsa
81