Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Seite 81

Miyambi ya Patsokwe Kanthu n’kako, kobwereka sikalimba m’chiuno. -Zinthu zobwereka zimakhala zosadalirika, choncho ndi bwino kumasamala chimene wabwereka kuti ukachibweze chili bwino. Kanthu n’kako, waona adakhuta thope. -Tisamafulumire kusiya kuchita chinthu chimene chingatithan- dize kukhala ndi tsogolo labwino monga sukulu. Kanthu n’kavumbu, kadavumbula mende pachisa. -Chinthu china chimatha kuululitsa chinthu china chomwe chi- nali chobisika. Kanthu n’kugwirizana, fisi adam’landa mbuzi. -Kuthandizana n’kofunika. Ukamachita zinthu limodzi ndi an- thu ena mogwirizana mumatha kupanga zambiri. Kanthu ndi khama, phwiti anakwatira njiwa. -Ngati titakhala ndi khama tikhoza kuchita zinthu zazikulu. Kanthu umaona, chilungulira ndi nthenda. -Tikangomva m’thupi kupweteka timangoti ndi malungo. Tiz- iyamba tadziwadi chimene tikudwala tisanamwe mankhwala. Kanyambitira sikanafe. -Mawuwa amanena za munthu amene akukakamira khalidwe lopanda pake, monga kuledzera, kuba komanso kutukwana. Pamapeto pake munthu wotereyu amadzakumana ndi mavuto aakulu mwinanso kufa kumene. Kaomba nkhadze n’kena, ithobwa otsata kuusa m’mthunzi. -Nkhadze ukaithyoka imatulutsa mkaka umene ungachititse kuti munthu achite khungu. Zochita za ana monga kuika mwala panjira zingabweretse mavuto komanso zingachititse ngozi. Kaphovu walowa m’dzombe. -Anthu oipa akamakhala pamodzi ndi anthu abwino, ama- pangitsa kuti abwinowo azioneka oipa. 80