Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 80
Miyambi ya Patsokwe
Kanthu kali m’mwayi, m’kamwini mnzanga wadya phiko.
-Anthu ena amakhala ndi mwayi pagulu kapena pamudzi.
Kanthu kali munye.
-Munthu umadziwa zinthu kuchokera kwa ena. Mwachitsanzo,
kuti udziwe nkhani inayake zimadalira kuti ena akuuze.
Kanthu kalikonse m’chifuniro, Buluzi anakana bweya.
-Munthu aliyense ayenera kumakhala ndi ufulu wochita zimene
akufuna.
Kanthu kandikhalira pamphuno.
-Mawuwa amanenedwa munthu akakumana ndi mavuto omwe
palibe chimene angachite kuti awathetse. Zimakhala ngati vuto-
lo lamuyandikira kwambiri moti palibe chimene angachite kuti
alimbane nalo.
Kanthu kavumbu ndi m’manja, m’magona mosambasamba.
-Pamoyo wathu tizikhala okonzeka kukumana ndi zilizonse
zotigwera, monga matenda komanso zina zosayembekezereka.
Kanthu koyambira sikachedwa kuoneka.
-Anzathu akatilangiza pa nkhani inayake tiyenera kuchita
kapena kusintha, tisamazengereze chifukwa zimadzaonekadi.
Kanthu n’kako uvundukura nupenya.
-Zinthu zako suziopa. Ukhoza kuchita nazo chilichonse chimene
ukufuna.
Kanthu n’kako, kamwini kadalira madzi.
-Zinthu zako suziopa. Ukhoza kuchita nazo chilichonse chimene
ukufuna popanda kuopa aliyense.
Kanthu n’kako, kamwini n’kamwini.
-Zinthu zako suziopa. Ukhoza kuchita nazo chilichonse chimene
ukufuna popanda kuopa aliyense.
79