Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 8

Miyambi ya Patsokwe kwa makolo ndipo makolowo ndi amene amavutika nalo. Akuluakulu saika mtima pa imfa yako, nawenso umwalira posachedwa. -Osamafunira mnzako zoipa chifukwa nawenso zikhoza kuku- chitikira. Akunja n’kunkhokwe. -Anthu ochokera kwina amakhala ngati nkhokwe chifukwa am- abwera ndi zachilendo. Si chinthu chanzeru kumanyoza anthu adera chifukwa nthawi zina ndi amene angatithandize kuthetsa mavuto athu. Akupempha, kali kutsaya. -Mawuwa amanenedwa pamene munthu akupempha chikhulu- lukiro kusonyeza kulapa koma n’kumapitirizabe kuchita zoipa. Akupempha, lumo lili kumutu. -Mawuwa amanenedwa wina akamalapa kapena kupepesa zin- thu zitavuta kale. Akuthawa mfuu yake yomwe. -Mawuwa amanenedwa ngati munthu akukana ntchito kapena cholakwa chomwe wachita. Mwachitsanzo mnyamata angakane mtsikana amene wamuchimwitsa (popeza onse amakhala achimwa mwina tinene kuti wachimwa naye). Alendo akaipitsa m’nyumba, m’mawa agona kuti? -Si bwino kuwononga zinthu pamalo amene tikukhala tikumaganiza kuti sitikhalitsapo, chifukwa mawa tidzafunanso kugona pomwepo. Ali dere n’kulinga utayenda naye. -Munthu umadziwa bwino makhalidwe a mnzako ngati utakha- la naye limodzi kapena kuyenda naye. 7