Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 79
Miyambi ya Patsokwe
Kangaonde kalira mtembo.
-Munthu aliyense ayenera kumalemekezedwa, osayang’ana
mmene alili.
Kangaonde kamakoma ndi mchere.
-Zinthu zooneka monyozeka zimatha kukhala zosililika chifu-
kwa chowonjezera tina n’tina.
Kankhuku kachilendo sikachedwa kugwidwa.
-Chinthu kapena munthu wachilendo pamalo nthawi zambiri
amadedwa. Chilichonse chikalakwika amati wachititsa kapena
wachita ndi iyeyo.
Kansalu kakafupi, malamulo tho!
-Mwambiwu unayamba chifukwa cha khalidwe la amuna ena
omwe amagulira akazi awo nsalu yosakwanira n’kumalongolola
kapena kukhazikitsa malamulo ambirimbiri. Osamavuta kwam-
biri tikhala ndi zinthu kapena tikachita chinachake.
Kanthu kakakhala kako, sikaneneka.
-Ngati nkhani ikukukhudza, si chapafupi kuinena. Ambiri
zikatero amangokhala du!
Kanthu kali kuchala.
-Kuti udziwe za chinthu, uyenera kuuzidwa ndi amene aku-
chidziwa bwino.
Kanthu kali m’makonda Buluzi akhumbira khonde.
-Zokonda zimasiyanasiyana, choncho mnzathu akamakonda zi-
nazake, tisamuseke chifukwa zokonda zathunso zikhoza kukha-
la zoseketsa kwa anthu ena.
Kanthu kali m’malira, Kalulu adalilira makutu.
-Pofunsira ntchito kapena mbeta munthu azisankha yekha
m’malo momusankhira chifukwa makonda amasiyanasiyana.
78