Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 78
Miyambi ya Patsokwe
Kandimverere adamva zam’maluwa.
-Ngati tikukayika kapena sitikudziwa zoyenera kuchita ndi
bwino kufunsa kuti tichite zinthu moyenera.
Kangachepe n’kachipongwe.
-Tisamaikire kumbuyo munthu wolakwa chifukwa cha msinkhu
wake. Si onse amene amachita chilungamo komanso chipongwe
sichichepa.
Kangachepe n’kang’oma, mkulu saomba chitsa.
-Tizikhutitsidwa ndi zomwe tili nazo kapena tapatsidwa.
Mwachitsanzo, munthu wopemphetsa samafuna kuti amupatse
zodzadza thumba.
Kangachepe, fungo n’lamake.
-Anthufe timatengera makhalidwe ena kuchokera kwa makolo.
Komabe, tiyenera kayesetsa kuchita zomwe tingathe kuti
tisinthe makhalidwe oipa.
Kangachepe, kako n’kako ndithu, kamwini sakandira.
-Kanthu kako ukhoza kukagwiritsa ntchito m’mene ukufunira
koma kamwini ayi.
Kangakanga adathyola nyani mchira.
-Si bwino kumaganiza kuti ukhoza kukwanitsa kuchita chili-
chonse wekha chifukwa ukadzapeza mavuto udzasowa
wokuthandiza.
Kangakanga anathyola nyau.
-Si bwino kumaganiza kuti ukhoza kukwanitsa kuchita chili-
chonse wekha chifukwa ukadzapeza mavuto udzasowa
wokuthandiza.
Kangakanga kanakanga.
-Si bwino kuti munthu udzikhala wodzikonda kapena woumira
chifukwa tsiku lina zikadzakuvuta umadzasowa wokuthandiza.
77