Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 77
Miyambi ya Patsokwe
mopupuluma.
Kampango woyera kumimba.
-Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene akukana mlandu
ponena kuti, “Ndilibe mlandu ndi munthu chifukwa palibe um-
boni wokwanira.”
Kamtande alemba pali khola.
-Munthu akakhalitsa kapena kuima penapake kwa nthawi
yaitali, ndiye kuti akudikira chinachake.
Kamtengo kamwana n’kamene amaphera njoka.
-Anthu anzeru amatha kulephera kuchita zinthu zing’onoz-
ing’ono, amawathandiza ndi anthu amene amaoneka ngati
opanda nzeru.
Kamtsitsi kadagwetsa abambo.
-Osachepetsa tchimo kapena cholakwa. Tiyenera kulapa chifu-
kwa lingadzatipezetse mavuto m’tsogolo.
Kamwana m’chokere, ukulu n’kuona kako.
-Mawuwa amanenedwa pakakhala chakudya chochepa. Ama-
sonyeza kuti ngakhale chakudya cha mwana, munthu ukhoza
kukhuta. Ndi bwino kumavomereza zinthu zikavuta.
Kamwini kalibe nkhoko m’nkhali.
-Munthu ukapita kwa eni, sumajijirika mpaka kufika pomauza
anthu kuti, “Tisunge chakudya chinachi kuti tidzadye m’mama-
wa.” Kapena kumakanganirana nawo zakudya zomwe zinatsala
dzulo. Ndi bwino kumakhala munthu woupeza mtima tikakhala
kuchilendo.
Kandimverere adakanena za m’maluwa.
-Zongomva chabe sizikhutiritsa. Pamafunika pakhale umboni
womveka bwino, apo ayi ndiye umafunika kupita komweko
kuti ukadzionere ndi maso ako.
76