Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 76

Miyambi ya Patsokwe Kamba amanyerera amene wamtola. -Pali anthu ena omwe umati ukawathandiza amabweza chipong- we kapenanso kukubweretsera mavuto. Kambalame kam’kamwa sikanona. -Anthu ambiri sakonda kucheza ndi munthu wolongolola ndipo nthawi zambiri munthu wotereyu amakhala wopanda khalidwe ndipo anthu amamuthawa. Kambalame kolawira kadakhuta nyongolotsi. -Tikamayesetsa kuchita zinthu moyambirira, monga kulimba munda, timapeza mphindu lalikulu. Koma ngati tayamba mochedwa, timakumana ndi mavuto ambiri n’kupeza phindu lochepa. Kambaleme kochenjera sikachedwa kukoledwa paulimbo. -Kuchenjeretsa komsamva nako malangizo kumaika munthu pa- mavuto aakulu ngati mmene zimakhalalira ndi mbalame yomwe imangoti zungulizunguli. Pamapeto pake imapezeka yakatera paulimbo. Kambuku sangasinthe manga ake. -Zimakhala zovuta kuti munthu asiye zinthu zimene anazolow- era. Kambuzi kapambuyo kadalinda mkwapulo. -Kuchita zinthu mochedwa kumapezetsa mavuto. Zimakhala ngati mbuzi imene ili m’mbuyo, munthu akamafuna kukwapula amakwapula imeneyoyo. Ndi bwino kumakhala patsogolo pochita zinthu. Kamodzikamodzi ndi mtolo. -Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi zinthu zing’onozing’ono. Mwambiwu umatiphunzitsanso kuti kuchita zinthu mwachifatse n’kothandiza kusiyana n’kuchita zinthu 75