Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 73
Miyambi ya Patsokwe
Kako n’kako, kamwini sakandira.
-Ukabwereka chinthu, sukhala ndi ufulu wochigwiritsa ntchito
mmene ukufunira. Ngati ukufuna kumagwiritsa ntchito chinthu
momasuka, ndiye ungachite bwino kungopeza chako.
Kako ndi ako kali m’mimba, kali padera si kako.
-Munthu uziwerengera chimene uli nacho, osati chomwe uku-
ganiza kuti ungadzakhale nacho.
Kako ndi ako wadya.
-Si bwino kutenga zinthu zimene si zako. Chomwe munthu
wadya ndiye chako chenicheni chifukwa palibe angakulande.
Kako sikanunkha.
-Umateteza abale ako komanso anzako. Anthu akamawanenera
zoipa, umawakometsera ngakhale zitakhala kuti amachitadi zin-
thuzo.
Kakonda mnzako mlekere, mawa kakonda iwe.
-Osachita nsanje ndi zinthu kapena mwayi wa ena, mawa ukho-
za kudzakhala mwayi wako.
Kakudza kokha kamalaula.
-Kuti upeze chinthu chabwino umayenera kuchivutikira. Chin-
thu chongobwera chokha n’chosadalirika. Choncho, si bwino
kukhala munthu waulesi.
Kale silibwerera.
-N’kupanda mnzeru kumalilira zakale. Ndi nzeru kumaganizira
za mawa mmalo momataya nthawi kuganizira zinthu zomwe
zinachitika kale ndipo sungazisinthe ngakhale pang’ono.
Kali kokha n’kanyama, tili awiri n’tianthu.
-Kukhala awiri si mantha, mumathandizana nzeru. Koma mun-
thu wokonda kuyenda yekha kapena kuchita zinthu payekha
72