Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 72
Miyambi ya Patsokwe
chake m’pofunika kumasamala ndi zimene timayankhula kuopa
kuyambitsa chipwirikiti.
Kagwa m’maso ndi kako.
-Osamawerengera zinthu zimene sunazilandire, mwina sizib-
wera. Chomwe uli nacho ndiye chako.
Kagwa m’maso tola.
-Mwambiwu ukunena za wakuba amene amatenga chilichonse
chomwe waona.
Kaitana kavula, ukachedwa ukakapeza katabopha.
-Ukaitanidwa umafunika kupita mofulumira, chifukwa
ukachedwa umakapeza zimene amakuitanirazo zitatha. Kuchita
zinthu panthawi yake komanso mosazengereza pamene wai-
tanidwa n’kofunika kwambiri. Ukachedwa umakapeza zatha
kale.
Kaitana kavula, ukachedwa upeza katavala.
-Ukaitanidwa umafunika kupita mofulumira, chifukwa
ukachedwa umakapeza zimene amakuitanirazo zitatha. Kuchita
zinthu panthawi yake komanso mosazengereza pamene wai-
tanidwa n’kofunika kwambiri. Ukachedwa umakapeza zatha
kale.
Kakachenjeretsa sikanona.
-Nthawi zambiri amene amakonda kuyankhulayankhula kapena
ochenjeretsa amakhala opanda nzeru. Chimodzimodzinso okon-
gola, amangokongola nkhope koma n’kukhala opanda nzeru
kapena opanda khalidwe.
Kako n’kako, kamwini katukwanitsa.
-Kanthu kako ukhoza kukagwiritsa ntchito m’mene ukufunira
koma kamwini ayi.
71