Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 71

Miyambi ya Patsokwe amaganiza kuti ndi amene achita zoipa. Tisamaweruze munthu potengera maonekedwe kapena potengera zimene anachita m’mbuyomu. Komanso munthu akakhala woipa kapena woch- enjeretsa amasowa mtendere, chifukwa chilichonse choipa amangoti wachita ndiwe. Kadyole pamzinda adathetsa anzake. -Kusyasyalika kapena kuti kuuza munthu zinthu zonama n’cholinga choti umusangalatse kungangoonongetsa zinthu. Ndi bwino kumauza anthu chilungamo koma mwachikondi. Kadzidzi amalemekeza nkhalango yake. -Aliyense ali ndi zinthu zimene zimamuthandiza komanso ku- chititsa kuti azilemekezeka. Kadziwa mwini mpeni wa m’chiuno. -Sitingathe kudziwa zambiri za anthu ena monga maganizo, mavuto kapena madandaulo awo. Kadziwa mwini msampha wa m’chipeta. -Ndi munthu amene watchera msampha mu udzu kapena kuti m’chipeta amene amadziwa pamene uli. Choncho, sitingathe kudziwa zambiri za anthu ena monga maganizo, mavuto kapena madandaulo awo. Kadziwa mwini nkhuto wa Fulu. -Sitingathe kudziwa zambiri za anthu ena monga maganizo, mavuto kapena madandaulo awo. Kadzola fumbi kalekeni, kali ndi nyimbo. -Munthu akayamba kuchita zinazake ndiye kuti pali chimene chikumulimbitsa mtima. Kagwa m’khutu satong’ola, atong’ola n’kam’maso. -N’zosatheka kubweza mawu atayankhulidwa kale. N’chifukwa 70