Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 70

Miyambi ya Patsokwe Kachipande katherere kamakoma n’kuyenderana. -Anthu amene amakhala bwino amafunika kumayenderana ko- manso kupatsana zinthu. Amafunikanso kuthandizana zikavuta, m’malo momangoyembekezera kuti munthu m’modzimodzi azitichitira zabwino. Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi bwino kumuchitira zabwino. Kachirombo kofula m’njira katama mano. -Munthu aliyense pamene akuyamba kuchita chinthu, monga banja kapena kulima munda, amafunika kuona kaye ngati an- gakwanitse. Amafunikanso kuona ngati ali ndi zonse zofunika kuti akwaniritse chinthucho. Mwachitsanzo, si bwino kulilowa banja ukumadalira ena kuti adzakuthandiza kapena kumabere- ka ana ukuwerengera kuti amalume adzawaphunzitsa. Kadapota nyanga kamadya ndi mvumbi. -Tiziganizira za tsogolo lathu. Kanyama kena kankaopa mvula ndipo sikankatuluka kupita kukadya moti kanaonda. Ndiye mvula itatha kanapita kukaba chakudya ndipo kanaphedwa. Ka- kanadya bwino nthawi ya mvula bwenzi kali ndi moyo nthawi yosowa chakudya. Kaduka ka chinangwa. -Mawuwa amatanthauza nsanje. Chifukwa cha nsanje, chinangwa chikazulidwa sichiphukanso kuopa kuti anthu anga- bwerenso ndi kudzathyola masamba ake kuti akapange ndiwo (chigwada) kapena kudzachizulanso. Kaduwa kokongola kamakopa Njuchi. -Anthu amatengeka ndi zimene akuona. Mwachitsanzo, amuna amakopeka ndi kukongola n’chifukwa chake akazi amadziphoda kuti akope njuchi. Kadya n’kena mbiri n’nja Khoswe. -Pali anthu ena chifukwa cha maonekedwe awo anthu 69