Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 69
Miyambi ya Patsokwe
Kachaje sikachepa, kachepa n’kamalonda.
-Tiyenera kuthokoza tikapatsidwa zinthu mwaulere ngakhale
zitakhala zochepa. Koma ngati tagula ndipo zinthuzo
sizinakwane pa mlingo wake, tiyenera kudandaula.
Kachepa alibe bwalo, ali ndi bwalo ndi kangachepe.
-Si bwino kumaderera zimene wangopatsidwa, kumangothoko-
za.
Kachepa kayenda, kakafa n’kophika.
-Pochita cholakwa munthu umaona ngati chaching’ono. Koma
chikaululika chimasanduka chachikulu komanso chochititsa
manyazi.
Kachepa n’kovala, kakudya sikachepa.
-Chovala chimodzi simungathe kuvala anthu awiri nthawi
imodzi. Koma chakudya ngakhale chitachepa bwanji mukhoza
kugawana. Mawuwa amanenedwa poitanira ena kuti adzadye
nawo chakudya.
Kachepa, n’kuona msandulizo.
-Vuto limachepa ngati tili ndi ena omwe angatithandize.
Kachepera maso, kamwa lilanda.
-Pali zinthu zina monga chakudya, milandu, zomwe poziona
zimakhala ngati zochepa koma kuti tizidye kapena kuzikamba
zimakhala zazikulu. Tisamaderere zakudya kapena kunyozetsa
nkhani.
Kachinyiza anang’amba thumba.
-Si bwino kukakamiza wina kuchita chinthu chomwe sakufuna,
chifukwa mapeto ake timapezeka tawononga, m’malo mokonza.
Kachinziri kamatupa patsala lake.
-Munthu amamasuka akakhala kwawo. Akhoza kudya kapena
kuchita zinthu zomwe kukanakhala kuchilendo sakanachita.
68