Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 68

Miyambi ya Patsokwe Jekete sapisira. -Mawuwa anganenedwe ngati wina wachita zinthu zabwino kwambiri moti sitingachitirenso mwina koma kumuyamikira. Anganenedwenso ngati wina akuyesa kuchita zosatheka. Tisamachite zinthu zosagwirizana ndi chizolowezi chathu, mon- ga kupisira jekete. Jelasi siipindula. -Njiru kwake n’kuwongonga zinthu komanso kubwezera zinthu m’mbuyo. Palibe chimene munthu angapindule ngati atamachi- ta jelasi. 67