Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 66
Miyambi ya Patsokwe
wakuba ali m’modzi yekha. Kulakwa kwa munthu wina kukho-
za kukhudza anthu ena.
Ili ndi amake simagwa m’mbuna.
-Anthu amene amalangiza ana awo ndipo anawo namvera
malangizo awo, kawirikawiri amakula bwino popanda mavuto
ambiri.
Iliko nja usiku, mkamwini anajiwa dzanja.
-Si bwino kuyembekezera zinthu chifukwa zikapanda kubwera
timadzagwira njakata.
Imfa ilibe odi.
-Imfa siipanganika, imabwera nthawi yosayembekezereka.
Choncho, timafunika kukonza moyo wathu wauzimu kuti
tikhale ndi tsogolo labwino.
Imfa siisankha, imatenga mkulu ndi mwana yemwe.
-Aliyense azikhala wokonzeka kuti tsiku lina adzamwalira.
Imfa siona nkhope.
-Imfa potenga munthu siyang’ana kuti uyu ndi ndani.
Imfa sithawika.
-Ngakhale munthu atachita zotani kuti asamwalire, mapeto ake
amafabe.
Ine-ine sin’theka pofula uchi.
-Si bwino kumangomva zathu zokha komanso kumamva
malangizo a ena ndinso kugawana nawo zomwe tili nazo. Um-
bombo suthandiza.
Ine-ine, sindim’tenga.
-Si bwino kumachita zinthu modzikonda pamalo, mapeto ake
umataya mwayi wopeza zabwino. Anthu sagwirizana ndi mun-
thu amene amachita zinthu modzikuza.
65