Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 65
Miyambi ya Patsokwe
Idakula nyanga poopa malunje.
-Kuti munthu akule ndi moyo ndiponso makhalidwe abwino,
ayenera kumalemekeza akuluakulu ndiponso kumadzisamalira
monga nyama imene imakula nyanga poopa kuyenda m’nk-
halango.
Ikachuluka pakamwa, siipenya pathumba.
-Pantchito pakachuluka anthu, ntchito siyenda, mmalo mwake
zimachuluka ndi nkhani.
Ikadza njala, umadya kontho.
-Munthu ukakhala pamavuto umachita zinthu zomwe
sungachite uli pamtendere.
Ikadza njala, usamataye gaga.
-Munthu aliyense amafunika kusamalira chuma chake, chifukwa
akachiwononga, tsiku lina amadzachifuna akadzakhala pa-
mavuto.
Ikadza njala, usamataye mtondo.
-Munthu aliyense amafunika kusamalira chuma chake, chifukwa
akachiwononga, tsiku lina amadzachifuna akadzakhala pa-
mavuto.
Ikakuthawa imawawa nsuzi.
-Munthu wina anagwira Njiwa ndipo anasangalala kwambiri
chifukwa ankadziwa kuti nsima ya tsiku limenelo ikayenda. Ko-
ma ali mkati moganiza zimenezi, Njiwayo inamupulumuka
n’kuthawa. Munthuyo anapsa mtima n’kuyamba kuikuwira
Njiwayo n’kumaiuza kuti, “Iweeeeeeeee, umawawa msuzi!”
Phunziro ndi lakuti osamanyoza chinthu chikapita.
Ikaola imodzi, zawola zonse.
-Pamudzi munthu akakhala wamakhalidwe oipa monga waku-
ba, anthu amangoti mudzi wonse ndi wa anthu akuba ngakhale
64