Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 63
Miyambi ya Patsokwe
kuyankhula chimene akufuna. Vuto limakhalapo ngati atachita
zinthu zophwanya malamulo.
Gulo akasowa mtengo, amazungulira chitsa.
-Pamlandu munthu ayenera kugwiritsa ntchito umboni uli-
wonse umene uli nawo. Chimodzimodzinso pamoyo wathu,
ngati tasowa chinthu tiyenera kupeza china choti chilowe
m’malo mwake.
Gumula zikulake.
-N’zosavuta kupeza zolakwa za wina, kuwononga zinthu, ko-
manso kugwiritsa ntchito zomwe wina wapanga. Koma kuti
upange zako pamakhala matatalazi.
Gunda umvetse.
-Pofuna kudziwa zoona zenizeni, munthu umayenera kufunsa
kapena kuchita zinthuzo.
Gunya sasenda, amene wasenda wakhuta.
-Mukamadya mbatata, anthu anjala sasenda, akayamba kusenda
ndiye kuti ayamba kukhuta. Choncho, tikamagwira ntchito,
zomwe tingathe kusiya osazigwiritsa ntchito tisataye nazo
nthawi.
Gwada utame, ndikuuze chinapha mako.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamalimbikitsa mnzake kuti
asabise chomwe wabwerera, kuti akatero nayenso amuuze zin-
thu zina zachinsisi.
Gwada, umvetse.
-Pofuna kumvetsa kanthu kenake pafunika kudekha, kudzi-
chepetsa ndi kupempha kuti wina akuthandize.
Gwadugwadu ndiko chikulu, chilili ndiko kupusa.
-Kugwada pamene munthu wamkulu akuyankhula ndi ulemu
62