Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 62
Miyambi ya Patsokwe
zabwino nthawi zonse. Nthawi zina munthu amakumana ndi
mavuto.
Golo! kumtondo, kumunda kulibe ndime.
-Mawuwa amanena za munthu waulesi, yemwe amakonda
kudya koma n’kumakana kugwira ntchito.
Gomo likagumuka, zako umadyeratu.
-Pamavuto munthu amayenera kuchita chilichonse kuti adzipu-
lumutse.
Gona n’kuphe sali kutali.
-Mawa si kalekale, ngati mmene zimakhalira ndi munthu amene
wauzidwa kuti aphedwa mawa. Nthawi imadutsa mofulumira
kwambiri.
Gona n’kuphe sikutali.
-Mawa si kalekale, ngati mmene zimakhalira ndi munthu amene
wauzidwa kuti aphedwa mawa. Nthawi imadutsa mofulumira
kwambiri.
Gonu, kwacha; masiku adyana.
-Munthu aliyense ayenera kukhala wokonzekera kugwira ntchi-
to chifukwa zamawa sizidziwika.
Gule aliyense amakoma potsiriza.
-Chinthu chilichonse chimakhala chovuta komanso chosasan-
galalatsa ukamachiyamba. Koma ukachizolowera chimayamba
kukusangalatsa.
Gule n’guleje, umakumbuka podya nkhwani.
-Osamakomedwa ndi zosangalatsa za m’dzikoli n’kufika poiwa-
la Mulungu kapena kuiwala zoti ukhoza kukumana ndi mavuto
kapena kufa kumene.
Gule ndi wa aliyense, kulakwa n’kuthyola mwendo.
-Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala, kuchita komanso
61