Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 61
Miyambi ya Patsokwe
ngati mmene amachitira Galu amene anasochera ndi goli lake.
Galu wakuba amaipitsa mbiri ya ana ake.
-Zimene munthu m’modzi angachite zikhoza kuipitsa mbiri ya
mtundu wake wonse kapena banja lake.
Galu wamiliri anaba nyama n’kuoloka nayo mtsinje.
-Munthu wopirira ndi amene amapindura nthawi zambiri. Kha-
ma limathandiza kuti munthu apeze chomwe akufuna.
Galu wamiliri anaoloka mtsinje.
-Munthu wopirira ndi amene amapindura nthawi zambiri. Kha-
ma limathandiza kuti munthu apeze chomwe akufuna.
Galu wamkota sakandira pachabe.
-Akuluakulu akamatichenjeza ndiye kuti alinga ataona kuopsa
kwa zimene tikuchitazo. Choncho, ndi bwino kumawamvera
kuti tipewe mavuto. Mwachitsanzo, galu wamkota, san-
gangokanda popanda kanthu. Mutafufuza mukhoza kupeza
kuti pali nyama.
Galu wandifera m’khwapa.
-Mawuwa amaneneda potanthauza kuti zangovuta koma tinaye-
setsa.
Galu wofewerera anapita ndi khongozi (goli).
-Munthu akakhala wotengeka ndi zonena za ena komanso
madandaulo a ena amasochera.
Galu wouwa saluma.
-Munthu woyankhulayankhula nthawi zambiri amakhala
wopanda mnzeru kapena wopanda mphamvu.
Gola akasowa Nkhuku, amatola udzu.
-Gola kapena kuti mphamba, imakonda kugwira Nkhuku. Ko-
ma zikavuta, imatha kudya udzu. Tisamangoyembekeza
60