Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 60
Miyambi ya Patsokwe
Galu adaipitsa yekha alendo.
-Mwambiwu umanena za munthu amene wadziwonongera
tsogolo pochita zinthu zosayenera.
Galu akati phethi, wataya nyama.
-Pogwira ntchito kapena pochita chinthu chilichonse, monga
maphunziro, sipamafunika kuyang’ana m’mbuyo kapena
kugwa mphwayi koma kudzipereka ndi mtima wonse. Ukapusa
umapezeka kuti wataya mwayi.
Galu ndi galu basi.
-Munthu amene ali ndi khalidwe kapena chizolowezi
chinachake zimavuta kuti asinthe.
Galu sasowa mbuyake.
-N’zofunika kuti nthawi zonse tizikumbukira amene amatithan-
diza, monga makolo ndi ena makamaka tikakhala pabwino.
Galu sauwa fupa lili m’kamwa.
-Anthu ena akakhala pabwino amaiwala za umphawi wawo
ndipo sasamala za anzawo.
Galu ukam’ponyera mafupa, sachoka pakhomo.
-Munthu ukakhala woolowa manja kapena wamsangala, anthu
satha phazi pakhomo pako.
Galu umamudzuma asananye.
-Munthu akayamba kuchimwa kapenanso zinthu zikama-
lakwika, timafunika kumuthandiziratu zinthu zisanafike poipa.
Galu wa mfumu ndi mfumu ya Agalu.
-Amene ali m’maudindo ena monga nduna, amaimira mtsogo-
leri wamkulu, choncho ngakhale atakhala kuti samatsuka
m’kamwa, timafunikabe kumawalemekeza.
Galu wadyera (wolusa) anapita ndi goli lake.
-Tisamachite chinthu ndi mtima wongofuna kusangalatsa ena
59