Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 6

Miyambi ya Patsokwe Akakhala mfulu ndi matenda, koma kapolo ndi ulesi. -Chinthu chimodzi chomwecho chimatchulidwa mosiyasiyana malinga ndi anthu ake. Munthu wolemera akhoza kutenga chin- thu cha mwini n’kumati anangolakwitsa. Koma akakhala wo- sauka amati waba. Akam’meta n’kumva wapinama. -Anamwali amaoneka ngati omvera komanso ofatsa ak- amapatsidwa malangizo. Koma akangomaliza kuwapatsa malangizowo, amakayambiranso makhalidwe awo oipa. Amai- walilatu zimene analangizidwa zija. Mwambiwu umanena za anthu amene samvera malangizo. Akalangizidwa amakhala nga- ti amva, koma pakangopita nthawi amayamba kuchitanso zom- we zija. Akapsala sagulitsana nkhwangwa yoduka. -Akamberembere sangapusitsane okhaokha. Mwachitsanzo, si kawirikawiri akuba kuberana okhaokha. Akapsala sapisana m’thumba. -Nthawi zambiri, anthu a makhalidwe ofanana sangapusitsane. Mwachitsanzo, si kawirikawiri akuba kuberana okhaokha. Akayanjana aleke. -Anthu amene amagwirizana nthawi zina amatha kuyambana kapena kudana kumene. Zikatere chimene chimafunika ndi kuyesetsa kuchita zinthu zoti agwirizanenso. Akoma akadadza. -Anthu amene poyamba amasonyeza makhalidwe abwino ke- nako n’kuonetsa khalidwe lawo lenileni. Akugwira ziputu. -Mawuwa amanenedwa mophiphiritsa za munthu amene aku- kana kuchoka pamalo kapena amene akukana kupita kumlandu 5