Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 59

Miyambi ya Patsokwe Fupa lokakamiza limaswetsa mphika. -Osakakamiza munthu kuchita zomwe sakufuna monga kukwa- tira, chifukwa akapeza mavuto akhoza kudzatiririra. Fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika. -Osakakamiza munthu kuchita zomwe sakufuna monga kukwa- tira, chifukwa akapeza mavuto akhoza kudzatiririra. Fwinyiririfwinyiriri adachedwa kudzuka, chinthu chidam’mb- wandira. -Kukhala fwinyiriri n’kudzipindabe pogona m’malo modzuka n’kumakagwira ntchito. Nthawi zina kukonda kwambiri chin- thu china kukhoza kutibweretsera mavuto, monga kungachitire kumangokonda kugona. 58