Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 57
Miyambi ya Patsokwe
Fisi akatola fupa sadyera pomwepo.
-Sibwino kumangouza aliyense za mwayi umene tapeza monga
udindo chifukwa angayambe kuona kuti ndife onyada.
Fisi akazingwa amadya udzu.
-Munthu ayenera kumakhutira ndi kangachepe kamene wapeza
akakhala pamavuto.
Fisi amakhalabe fisi, ngakhale atasintha tchire.
-Munthu woipa ndi woipa, sangasinthe chifukwa choti wasintha
malo. Chimodzimodzinso chinthu choipa, sichingasanduke
chabwino ngakhale utachichita pa zolinga zabwino.
Fisi atolapo tsoka.
-Munthu ukakhala wakhalidwe loipa monga kuba ndiye chinthu
n’kusowa pakhomo, anthu amangoti ndiwe, ngakhale palibe
umboni wokwanira wachitadi zinthuzo ndiwe.
Fisi ayamika ake maluwa.
-Munthu amakonda kuyamikira zinthu zake n’kumaona kuti
n’zabwino kuposa zonse.
Fisi ndi Mbuzi sizigonera limodzi.
-Mawuwa amanena za zinthu zomwe ndi zosayenera kukhalira
limodzi kapena kugwirizana. Mwachitsanzo, anthu odana, say-
enera kumakhalira limodzi chifukwa mapeto ake akhoza ku-
phana.
Fisi saopa mdima.
-Munthu amene amakonda zoipa saopa anthu kapena zinthu zo-
opsa ndi zonyansa. Amayendanso ndi anzake omwe ndi oipa.
Fodya amakoma ngokoketsana.
-Mawuwa amatanthauza kuti moyo wa munthu umakoma ndi
kugawana zinthu monga nzeru, zakudya, zovala ndi zina.
56