Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 56
Miyambi ya Patsokwe
Fisi adakana nsatsi.
-Si zonse zimene anthu amanenera munthu zimakhala zoona.
Ngakhale munthu atakhala wamakhalidwe oipa, pamafunika
umboni weniweni tisanamunene kuti wachita cholakwa.
Fisi adalira msampha utaning’a.
-Nthawi zina timataya mtima kapena kugwa mphwayi mavuto
athu atatsala pang’ono kutha. Tiyenera kupirira mpaka
pamapeto.
Fisi akafuna kuluma sasiya mkute.
-Ndi bwino kumangochitiratu chinthu m’malo mosiya zina kuti
udzachitabe.
Fisi akagwa m’mbuna sayankhula kanthu.
-Munthu akapalamula mlandu amafunika kungovomereza ndi
kupepesa m’malo momakula mtima. Mawuwa anganenedwenso
ngati munthu akusowa choyankhula akagwidwa ndi mlandu.
Fisi akagwa m’mbuna, mawa adzalandira nkhwangwa.
-Munthu akachita choipa, zivute zitani amakumana ndi mavuto
a zimene wachitazo. Choncho ndi bwino kungovomereza ndi
kupepesa m’malo momakula mtima. Mawuwa anganenedwenso
ngati munthu akusowa choyankhula akagwidwa ndi mlandu.
Fisi akagwira sataya.
-Munthu suyenera kutaya chinthu chimene umachidalira ko-
manso chimakuthandiza monga ntchito, chipembedzo ndi zina.
Fisi akakhuta salilira pomwepo.
-Pamene munthu wapeza mwayi wina, usamawanyang’wire
amene akupatsa mwayiwo monga makolo, aphunzitsi ndi aku-
luakulu a pantchito, chifukwa angakulande zomwe wapezacho.
55