Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 55
Miyambi ya Patsokwe
Dzungu m’gonera kumodzi.
-Mawuwa amanena za anthu omwe amangochita zawo. Safuna
kumva za ena kapena kugwirizana ndi anzawo.
Dzuwa likawomba, wotheratu.
-Mwayi ukapezeka, kapenanso ukakhala ndi nthawi, mpofunika
kuchitiratu zowe ukufuna kuchita, chifukwa mwina tsiku lotsa-
tira kudzakhala mitambo.
Dzuwa likung’amba mtengo.
-Mawuwa amanenedwa zinazake zikachitika poyera anthu
akuona.
Dzuwa likuwomba mtengo.
-Mawuwa amanenedwa zinazake zikachitika poyera anthu
akuona.
Dzuwa limanyenga, mdima umasaka.
-Pamene walakwira makolo masana, umatha kuthawa. Koma
kukada umapitanso kwa makolo ako n’kukalangidwa.
Cholakwa sichithawika, nthawi imafika ndipo munthu ama-
landira chilango cha zimene wachita.
Dzuwa salozerana, aliyense amaliona yekha.
-Pali zinthu zina zomwe sitimafunika kuchita kufotokozera
anzathu.
54