Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 54
Miyambi ya Patsokwe
ndalama. Amakonda kugwiritsidwa ntchito ndi amwenye omwe
amapanga bizinezi.
Dziko silimaipa, amaipa ndi anthu.
-Tisamaganize kuti tikachoka pamudzi wina n’kupita kwina
chifukwa cha kukangana ndiye kuti kukangana kwatha ayi,
chifukwa amene amayambitsa kukangana si malo, koma anthu.
Dzimvere mtolo.
-Mawuwa amanenedwa pouza munthu kuti wamva zimene
zanenedwa, kwatsala n’kuti azigwiritse ntchito.
Dzina silifa.
-Ana akabadwa amatsala ndi dzina la munthu amene ana-
wabereka.
Dzinena kuti mafano, udzafa maono adakayera.
-Mwambiwu umatanthauza kuti kunyoza malangizo a aku-
luakulu kapenanso zikhulupiriro zamtundu wako
kungakubweretsere tsoka. Mpofunika kumanyadzira chikhalid-
we chathu komanso kumamvera malangizo.
Dzino siliononga nyumba ya msonkhano, koma lirime.
-Chimene chimachititsa kuti anthu asiye kugwirizana kawiri-
kawiri silikhala dzino, koma pakamwa.
Dzira siliola tsiku limodzi.
-Khalidwe la munthu siliyamaipa tsiku limodzi. Ngati munthu
walakwa ndiye kuti anayamba kale kuchita zinthu zoipa,
kungoti sankagwidwa.
Dzungu limakula kunsonga.
-Nthawi zina munthu wobadwa pambuyo ndi amene amakhala
wamphamvu, wokula bwino ndiponso wanzeru kuposa wo-
yamba kubadwa.
53