Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 52
Miyambi ya Patsokwe
Dombolo n’kuwombolana, nthengu anaombola namfuko.
-Kuti anzako akuthandize pamafunika kuti nawenso uziwathan-
diza, osamangoyembekezera kuti anthu akuthandize.
Dombolo n’kuwombolana.
-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi bwino kumuchitira
zabwino. Zimakhala bwino kumathandizana.
Dothi sinkadakudya, ndakudyera ku uchi.
-Nthawi zina umathandiza munthu osati chifukwa choti
umamukonda, koma chifukwa choti umakondana ndi mnzake.
Dulani kachere pumbwa anyale.
-Anthu ena amanyada mwinanso kuzunza anzawo chifukwa cha
udindo, ndalama kapenanso makolo awo. Zinthu zotere zikatha,
kuzunza ndi kunyada kumathera pomwepo.
Dyera linapititsa Ntchentche kumanda.
-Kuchita zinthu mwadyera pa chilichonse, ngakhale chabwino,
kumatsekereza zabwino, monga kukwezedwa pantchito.
Dyeratu, chakudza sichinena.
-Munthu ngati uli ndi chuma uyenera kusangalala nacho chifu-
kwa zamawa sizidziwika.
Dzandioneni n’kukhala ndi zako.
-Osamadzitamira katundu wa eni ake koma wako.
Dzanja limodzi silikumba mankhwala.
-Kuthandizana n’kofunika popeza pawekha sungachite zinthu
zambiri.
Dzedzeredzedzere (dzandidzandi) salingana n’kugweratu.
-Kulephera sikutanthauza kuti sungakwanitse kuchita chinthu.
Kuti munthu achite bwino amafunika kukumana kaye ndi
mavuto.
51