Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 51
Miyambi ya Patsokwe
Dala la mwana wankhuku lolira make ali pomwepo.
-Anthu ena amangodandaulabe ngakhale kuti ali nawo anthu
owathandiza. Aliponso ena amene amavutika koma njira yothet-
sera mavuto awo akuidziwa.
Dala lidagoneka munda.
-Kulekerera kumawonongetsa zinthu. Ulesi si wabwino
mpang’ono pomwe.
Dama n’kumeta, mphini ndi chironda.
-Pofuna kuwonjezera kukongola kwa chibadwa, nthawi zina ti-
madziwononga potsata njira zosayenera.
Dengu lidawombola mbiya.
-Ndi bwino kumathandizana. Aliyense ndi wofunika pantchito
yake.
Dengu silidya.
-Nsengwa, dengu kapena bwato zimangosunga zinthu zimene
mwaikamo, sizimachepa kapena kuwonjezereka. Tizikhutira ndi
zimene tili nazo pamoyo wathu.
Dikira madzi apite, kenako uziti ndadala.
-Munthu ukakhala pabwino usamati ndadala, chifukwa ukhoza
kukumana ndi mavuto nthawi iliyonse.
Dingudingu amanena za mnzake, zake wapsindira.
-Pali anthu ena omwe amakonda kunena zoipa za anzawo
n’kusiya zawo. Munthu aliyense amayenera kumayamba waona
kaye zimene amachita asanayambe kunena za anzake.
Diso la Nkhwazi.
-Maso a Nkhwazi ndi akuthwa kwambiri omaona chinthu chili
patali. Mawuwa amanena za munthu amene amaona patali.
Diso likatuluka, ndi maliro.
-Maso a munthu akatuluka, ndiye kuti munthu wamalizika.
50