Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 50
Miyambi ya Patsokwe
Chulukechuluke ngwa njuchi, umaloza yomwe yakuluma.
-Pokamba nkhani pafunika kunena zenizeni m’malo momango-
zungulirazungulira. Mwambiwu umanenedwanso pakakhala
anthu ambiri amene akuganiziridwa kuti alakwa, koma
pamapeto pake amapezeka m’modzi. Ungatanthauzenso kuti
chimene chakudolola n’chimene umachitchula Ungatanthauzen-
so kuti chinthu chimene chimakuchititsa chidwi ndi chimene
ukuchidziwa bwino. Ngakhale patakhala zinthu zochuluka,
umanena za chimene chakuchititsa chidwi.
Chulutsa masamba, ungagwire nsete.
-Mwambiwu umanenedwa pouza munthu kuti achulutse
zonena kuti asagwidwe.
Chuma chili m’nthaka.
-Ukalimbikira kulima, udzapeza zofuna zako.
Chuma chimuka pa chuma chinzake.
-Anthu amene ali ndi chuma ndi amene amapeza chuma china.
Chuma chothamangira chimapatsa matsoka.
-Kususukira kulemera kungatipalasire moto.
Chuma ndi mchira wa khoswe, suchedwa kupululuka.
-Chuma sichichedwa kutha ngati mmene umachitira mchira wa
khoswe. Ukaugwira, umangopululuka. Ngati sukuchisamalira
bwino, chimatha chonse phu! Ukakhala pabwino usamanyoze
anzako chifukwa ndi amene angadzakuthandize ukadzavutika.
49