Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 5

Miyambi ya Patsokwe Adatha mphika ndi “n’talawa.” -Kukomedwa ndi chinthu kumapangitsa kuti uzolowere kenako umatha kupalamula. Adera amakoma podya nawo. -Anthu adera amakonda munthu akakhala pabwino koma zik- amuvuta kapena akasauka, amamuthawa. Achibale ake okha ndi amene amamusamalabe. Adye zabwino anadya zowawa. -Mwambiwu umachenjeza munthu amene amafuna atapeza zabwino zonse nthawi imodzi. Akapanda kusamala amatha ku- kumana ndi mavuto. Choncho, zabwino zimabwera pang’onopang’ono, munthu amangofunika kudikira kuti nthawi yake ifike. Adzidyera pamutu pa mfumu. -Nthawi zina munthu amapeza mwayi chifukwa cha munthu wina osati chifukwa cha khama lake lokha ayi. Agona chimwini nsomba. -Nsomba imakhala ngati yagona koma ikuona zonse zomwe zik- uchitika. Mwambiwu umanenedwa munthu wina akamakhala mosamala kapena akamagona makutu ali kunja poopa kuti ena akhoza kumuchita chipongwe. Akafuna kuchita, Kalulu azembera Galu. -Pali anthu ena omwe amati akachita choipa amayamba kunamizira osalakwa kapena omwe nkhaniyo sikuwakhudza. Nthawi zambiri anthu ngati amenewa amaoneka ofatsa. Zimene anthu oterewa amachita zikuyerekezedwa ndi zimene zingachi- tike ngati Kalulu wachita chinachake choipa koma mlandu n’kugwera Galu wosalakwa. 4