Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 49
Miyambi ya Patsokwe
wamunthu chifukwa nthawi zina pathawapo umakumana ndi
vuto lina lalikulu.
Chozingwa sichilira nkhata.
-Tikakhala pamavuto pafunika kuyamba kudzithandiza tokha
osamangoyembekezera kuthandizidwa ndi ena. Tikadzithandiza
tokha enanso adzatha kutithandiza.
Chule anadabwa m’madzi muli mwake.
-Pali zinthu zina zomwe zimachita kuonekeratu kuti sizimakha-
la choncho.
Chule anadabwa madzi atafika m’khosi.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamadabwa ndi zinthu zom-
we zimayenera kuchitika pamoyo wathu.
Chule wodzikuza adaphulika.
-Sibwino kumadzikuza chifukwa umatha kudzichititsa manyazi
pagulu.
Chulu sichiyendera chiswe, chiswe chimayendera chulu.
-Chithu ukachifuna umafunika uchite chinthucho.
Chulukechuluke n’ngwa njuchi, umanena za iyo yakuluma.
-Pokamba nkhani pafunika kunena zenizeni m’malo momango-
zungulirazungulira. Mwambiwu umanenedwanso pakakhala
anthu ambiri amene akuganiziridwa kuti alakwa, koma
pamapeto pake amapezeka m’modzi. Ungatanthauzenso kuti
chinthu chimene chimakuchititsa chidwi ndi chimene uku-
chidziwa bwino. Ngakhale patakhala zinthu zochuluka,
umanena za chimene chakuchititsa chidwi.
Chulukechuluke ngwa chambo, doko n’la ntchira (kambuzi).
-Ngakhale ogwira ntchito akhale ambiri, komabe, eni ntchito
kapenanso amene akugwira molimbika amadziwika.
48