Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 48
Miyambi ya Patsokwe
Chonona chifumira ku dzira.
-Maonekedwe ndi makhalidwe a munthu amakhala ochokera
kwa makolo ake.
Choopera patali, nyani anadzipha yekha.
-Si bwino kumangoopera chinthu patali.
Chosadziwa anausa mvula m’dziwe.
-Nthawi zina tikhoza kumaganiza kuti tikuthawa mavuto n’kud-
zilowetsa m’mavuto aakulu mmalo mongopirira n’kuyesa
kuthetsa vutolo. Mwachitsanzo, munthu amene wadzimangirira
amati akuthawa mavuto.
Chosadziwa ndi nkhondo, adausa nkhondo padziwe.
-Nthawi zina tikhoza kumaganiza kuti tikuthawa mavuto n’kud-
zilowetsa m’mavuto aakulu mmalo mongopirira n’kuyesa
kuthetsa vutolo. Mwachitsanzo, munthu amene wadzimangirira
amati akuthawa mavuto.
Chosamva adachiphikira m’masamba.
-Anthu amene samvera malangizo amakumana ndi zokhoma
kapena kufa kumene. Wina akakulangiza pamafunika kumvera.
Chosatha n’chiyani?
-Chilichonse chimatha pakapita nthawi.
Chotola salanda.
-Kutola kanthu si kuba, koma ukatenga pakhomo pa munthu
osapempha.
Chozemba chinakumana ndi chokwawa.
-N’kovuta kuthawa mavuto kapena milandu chifukwa nthawi
zina pothawapo umakumana ndi vuto lina lalikulu. Nthawi zina
munthu amazemba, koma tsiku lina amadzagwidwa.
Chozemba chinalinda kwawukwawu.
-N’kovuta kuthawa mavuto kapena milandu pamoyo
47