Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 47
Miyambi ya Patsokwe
Chizolowezi cha namkholowa chidazulitsa mbatata yapansi.
-Zinthu zina zimaululika chifukwa cha zinanso zimene zachi-
tika. Makhalidwe oipa monga chiwerewere ndi kuba amayamba
pang’onopang’ono. Pamafunika kudziletsa kuti usachite zinthu
zomwe mapeto ake akhoza kukhala kuchimwa kwakukulu.
Chizolowezi chidadya mzuzya.
-Zotsatira za zizolowezi zoipa ndi mavuto monga matenda,
milandu komanso imfa.
Chizolowezi chinalowetsa nsabwe kumutu.
-Ukamacheza ndi anthu ochita zoipa nawenso umayamba ku-
chita zoipa.
Choipa chitani mbiri siigonera.
-Mbiri imamveka msanga. Ngakhale utayesetsa kuimphimba an-
thu amamva. Koma sipapita nthawi amayamba kuiwala.
Choipa chitsata mwini.
-Palibe munthu amene angachite choipa n’kuthawa, tsiku lina
ndithu amadzakumana ndi zotsatira za zoipa zimene anachi-
tazo.
Choipa ndi mnyanga ya njovu.
-Munthu ukhoza kumachita zoipa n’kumaganiza kuti sichidzau-
luluka. Koma monga mnyanga ya njovu sitheka kuibisa,
choipacho tsiku lina chimadzaululika ndipo munthu
umadzalangidwa.
Choka m’mbuyo Khwangwala atole mphutsi.
-Umafunika kupereka mpata kwa anzako kuti akhale omasuka
pang’ono. Osamatsekereza mwayi wa ena.
Cholira Njovu chidalira minyanga.
-Aliyense ali ndi ufulu wogwira ntchito imene akufuna popanda
kukakamizidwa.
46