Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 46
Miyambi ya Patsokwe
kuwathandiza zili m’nkhonde. Mwachitsanzo, kumavutika ndi
njala dimba ali nalo.
Chitsiru chinaomba ng’oma, ochenjera navina.
-Nthawi zina anthu ooneka ngati opusa ndi ofooka amatha ku-
chita zodabwitsa motero kuti anthu odziyesa ochenjera n’kuten-
gerapo phunziro.
Chitsiru chinaona nkhondo.
-Si bwino kunyoza munthu chifukwa santha kuchita zinthu zina.
Nayenso akhoza kukhala ndi mbali ina yomwe amachita bwino.
Chitsiru nachonso chili ndi amake.
-Ana kapena ziweto zimadziwa makolo komanso mbuye wawo.
Munthu sulephera kuzindikira chinthu chako.
Chitsulo chimanola chitsulo chinzake.
-Anthu ochita zofanana amathandizana. Kuti munthu akhale ndi
luso amayenera kumatengera anzake.
Chitukuko ndi kupirira.
-Kuti atsikana kapena azimayi atchene, kaya ndi m’mutu, ama-
funika kupirira ululu. Mwachitsanzo, ena amapsa ndi livuloni
koma samasiya.
Chiwindi cha Nkhandwe chalaka mwini msampha.
-Chomwe chakanika munthu wakale kapena wanzeru, mwana
sangachithe.
Chiyipira achaje, amake amati mwana.
-Ngakhale anthu ena atamanyoza munthu chifukwa cha maon-
ekedwe kapena khalidwe lake, makolo ake ndi abale ake ama-
mukonda, sangamutaye kapena kumunyoza.
Chizolowezi cha namkholowa chidaululitsa mbatata.
-Si bwino kuchita khalidwe loipa chifukwa likhoza kukubwer-
etsera mavuto.
45