Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 45

Miyambi ya Patsokwe Chithupsa chosatumbula sichigonetsa tulo. -Munthu sangagone tulo ngati pali mavuto ena omwe akufunika kuwathetsa kapena amene akumusowetsa mtendere. Chithupsa chosatumbula sichigonetsa tulo. -Munthu ukapalamula kapena ukakhala ndi mlandu, mtima su- khala pansi, umada nkhawa mpaka mlandu utakambidwa. Chitoletole chidaphetsa manja. -Munthu wakuba tsiku lina amadzapezana ndi tsoka monga kudulidwa manja. Chitosi cha nkhuku yachilendo chimatalika. -Mlendo akafika pamudzi n’kulakwa, kulakwa kwake kumaon- ekera kwambiri ngakhale kuti nawonso eni mudzi amalakwa mwina kuposa mlendoyo. Chitsa chagwede chinagwetsa nkhalamba. -Kulakwa kwa ana kukhoza kusowetsa mtendere munthu wamkulu. Zochita za ana zimavutitsa akulu. Chitsime chakele chimaphetsa ndi ludzu. -Osamanyoza zinthu kapena anzathu akale chifukwa tsiku lina tidzawafunanso. Choncho ngati timawanyoza sadzatilandira. Mwambiwu ungatanthauzenso kuti tikasiya kuchita zoipa tifunika kuchita khama kuti tisabwererenso ku zochita zoipazo. Chitsime chimadziwika kuti ndi chakuya chikauma. -Munthu wabwino amadziwika akapita. Mwachitsanzo, ena amazindikira kuti mkazi kapena mwamuna wawo anali wabwino banja likatha. Nthawi zambiri amazindikira zimenezi akakwatirana ndi chilombo. Chitsiru chimafa ndi ludzu mwendo uli m’madzi. -Pali anthu ena omwe amavutika zinthu zoti zikhoza 44