Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 44
Miyambi ya Patsokwe
Chisoni chinapha Nkhwali.
-Nthawi zina chisoni chikhoza kukubweretsera mavuto. Nkhani
yake imati, kalekalelo Njoka inkafuna kuwoloka mtsinje wina.
Ndiye popeza palibe chimene ikanachita kuti iwoloke yokha,
inapempha Nkhwali kuti aithandize. Nkhwaliyo inamva chisoni
zedi ndi mmene Njokayo inkaonekera ndipo inavomera kuti
ichitadi zimene Njokayo inkafuna. Inauza Njokayo kuti,
“Zizengereze m’khosi mwangamu!” Kenako inanyamuka
n’kuuluka. Itafika kutsidya, Nkhwaliyo inauza Njokayo kuti,
“Bwanawe, tafikatu. Tsopano ukhoza kutsika kuti uzipita.”
Koma Njokayo inakana kwamtuwagalu kuti sichoka. Pamapeto
pake, chisoni chinachitsa kuti Nkhwali ione tsoka la nkhuku.
Chisoni chinapha nsemamitondo.
-Munthu amene umamuthandiza poganizira kuti akusowa
thandizo ndi amene amadzakuukira, mwinanso ngakhale kuku-
pha kumene.
Chisoni n’kumatenda, kumaliro kumakhala nkhani.
-Pamene munthu akudwala anthu amakhala ndi chisoni, koma
akamwalira, chisoni chonse chimatha popeza amadziwa kuti
palibenso chimene angachite. Mwina ena amayamba kukamba
mbiri ya womwalirayo, zabwino kapena zoipa.
Chiswe chikaboola chikwa, chayambira patali.
-Munthu ukakhala ndi cholinga n’kuchita khama, umapeza
zimene ukufuna. Ungatanthauzenso kuti vuto likamaonekera
ndiye kuti layambira patali.
Chiswe chimalowa m’mphasa yongoimika.
-Munthu waulesi amakumana ndi zovuta zambiri.
Chiswe chimodzi sichiumba chulu.
-Ngati titamathandizana tikhoza kugwira bwino ntchito zathu
mpaka kumapeto.
43