Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 43

Miyambi ya Patsokwe zabwino. Choncho, kuti anthu muthandizane pamafunika pa- khale ubale weniweni pakati panu. Chipande chomwe umawomorera mnzako, nawe adzakuwomorera chomwecho. -Ngati ukufuna kuti anzako azikuchitira chifundo, yamba ndi iweyo kuwachitira. Chipititsira m’ngunda. -Mwambiwu umagwiritsidwa ntchito pamene munthu wanena dala zosagwirizana ndi nkhani kuti asokoneze anthu, maka- maka pa mlandu. Chipungu sataya nthenga. -Mawuwa amanena za munthu waumbombo yemwe safuna ku- gawira anzake zinthu. Chipwete mpamtsitsi. -Chipwete chimakhala chaminga kuchokera ku mbewu. Chimodzimodzinso khalidwe la munthu limachokera kwa ma- kolo. Chirombo chinafera m’dambo la kamundi. -Chifukwa cha nsanje anthu ena amafuna kutchuka pantchito za eni mwina chifukwa choti anamwalira, komabe anthu amawadziwa ndipo mapeto ake amaputa nazo mlandu. Chisakomere Mbuzi kugunda Galu, Galu akaluma ati ndi woipa! -Pali anthu ena omwe amakonda kuchitira anzawo zinazake, anzawowo akawachitira zangati zomwezo amaona kuti awala- kwira kwabasi. Chisanakondwe chilonda njira, chikakondwa chachenjera. -Zotigwera zina zimatikumbutsa nsanga kumudzi koma pa zosangalatsa timachita ngati taiwalako. 42