Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 41

Miyambi ya Patsokwe chifukwa mapeto ake chimadzakhala chizolowezi n’kud- ziwononga tokha. Chimvano cha mavu choning’a pakati. -Ndi bwino kumachita zinthu mogwirizana. Ngakhale kuti pan- gano limavuta kusunga nthawi zina, komabe tiziyesetsa kusunga zomwe tagwirizana popewa kukhumudwitsa ena. China n’china Fisi alibe bwenzi, bwenzi lake ndi mdima. -Anthu ochita zoipa sakhala mabwenzi abwino, mabwenzi awonso amakhala ochita zoipa. Chinansi cha kholowa chinadyetsa mbatata yapansi. -Zinthu zina zimaululika chifukwa cha zinanso zimene zachi- tika. Makhalidwe oipa monga chiwerewere ndi kuba amayamba pang’onopang’ono. Pamafunika kudziletsa kuchita zinthu zom- we mapeto ake akhoza kukhala kuchimwa kwakukulu. Chinasala chinakanika Fisi. -Chinasala ndi chisilamu. Anthu achisilamu amasala nyama zi- na. Koma Fisi ndi wankhwiru kwambiri moti sangakwanitse kusiya kudya nyama ngakhale itakhala kapado. Pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kuzisintha chifukwa cha chibadwa chathu. Choncho, munthu ayenera kumadziwa zomwe angathe kuchita komanso zomwe sangathe. Chinenepetsa Nkhumba sichidziwika. -Ndi bwino kumangoyesa kuchita zosiyanasiyana, chifukwa chimene chingakupulumutse sichidziwika. Osamangodalira chimodzi. Chingaipe sunga, mkucha udzayesa ankhoswe. -Chinthu chingaipe, tsiku lina umadzaona pokomera pake. Chingavuwe n’chako. -Ngakhale anzathu kapena makolo athu akhale osaoneka bwino, 40