Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 40

Miyambi ya Patsokwe chifukwa tikamatero tikhoza kuiwala zinthu zofunika. Chimanga cha palikodza amakolola ndi Sakhwi. -Ndi bwino kumadziwa zinthu zomwe sungakwanitse. Pali zin- thu zina zomwe ngati utazikakamira kwambiri zikhoza kungokubweretsera mavuto ngati chimanga chomwe chili pali- kodza, lomwe ndi tchire loyabwa kwambiri. Ndi bwino kusiyira Asakhwi zinthu zimenezo. Chimanga chimalola opanda mano. -Nthawi zina munthu umapeza chinthu choti ulibe nacho ntchi- to pamene munthu wina akuchifunitsitsa. Chimasomaso chinakwatitsa mkazi wosam’funa. -Mnyamata wosakhala ndi mkazi m’modzi koma kumangoti apa wagwira apa wagwira, mapeto ake amadzakwatira mkazi wosa- khala wakumtima kwake, mwinanso kupeza mavuto. Chimene chakupundula chitsate, chikupatsa khongozo. -Munthu uyenera kudyerera chomwe wavutikira. Chimene ukufuna kuti ena akuchitire, iwenso uziwachitira chomwecho. -Kuti tizichitira ena zabwino, ndi bwino kumayamba taganiza kaye kuti, “Kodi wina atandichitira zimenezi ndingasangalale?” Ngati tikuona kuti sitingasangalale, tingachite bwino osazichita. Chimkonda cha nsikidzi chidanka ndi maliro kumanda. -Osamakonda zinthu zoipa monga chiwerewere, mowa kapena chamba chifukwa mapeto ake ndi imfa. Chimkwangukwangu chisititsa makadabo. -Kulimbirana zinthu kukhoza kuyambitsa ndewu kapenanso mkangano n’kuwonongetsa zinthu zambiri. Chimuyesoyeso cha Khwangwala chinathetsa ana. -Si bwino kuyesa kuchita zinthu zoipa monga kusuta chamba 39