Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 4

Miyambi ya Patsokwe Abwino sakhalitsa. -Anthu abwino sakhala moyo nthawi yaitali. Achimseka pachimera. -Mwambiwu umanena za anthu amene amakonda munthu aka- khala ndi chinachake choti awapatse monga zakudya, zakumwa kapena zinthu zina zomwe akudziwa kuti akhoza kupindulapo. Zinthuzo zikangomuthera amamutaya. Achimseka pamaso, mumtima muli zina. -Pali anthu ena omwe pamaso amaoneka ngati anzako, koma kumbali amakudya miseche kapena kukukonzera zoipa. Ena amakhala oti mumtima mwawo anakupha kalekale. Achoke malizagudu, tiyanike inswa ziume. -Mwambiwu umanenedwa ndi anthu omwe sakufuna kuti anzawo akhalepo akamachita zinazake. Mwachitsanzo, akhoza kukhala kuti akufuna aphike nsima koma sakufuna kuti anzawowo adye nawo. Zikatero amadikira kaye enawo achoke ndipo pouzana ndi amene amagwirizana nawo amati, “Dikirani kaye, achoke malizagudu, tiyanike inswa ziume.” Mwambiwu ukhoza kunenedwanso ngati wina akungofuna kuti achite zi- nazake anthu ena akachoka. Adadya Kalikongwe wa nzeru zayekha. -Mwambiwu umanena za munthu amene samvera malangizo. Nthawi zambiri munthu wotereyu amadzakumana ndi mavuto kapenanso kufa kumene. Nkhani yake imanena za mbewa yotchedwa Kalikongwe. Tsiku lina anzake ankaiuza kuti, “Usakhale apa anthu angakuphe,” koma Kalikongwe sanamvere. Anzakewo atachoka, kunabweradi anthu ndipo ata- mupeza anamupha n’kukamudyera nsima. 3