Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 39
Miyambi ya Patsokwe
lakelo n’kuliika munkhali n’kutenga madzi obwadamuka n’ku-
wakhuthulira momwe munali bulangetelo kuti nsikidzizo
zikhaule. Ndiye zimenezi zitangochitika, Nsikidzi yomwe inali
m’bulangetemo inauza ana ake kuti, “Ana anga, muyenera ku-
khala opirira, chifukwa chilichonse chotentha, pamapeto pake
chimazizira. Vuto lingatenthe bwanji, limakhala ndi mapeto
ake.” Mavuto angakule bwanji, amakhala ndi polekezera.
Chilimwe chinaphetsa munda.
-Munthu wofuna zabwino asamathawe zopinga monga kuuma
komanso kulimba kwa dothi, amafunika kupirira.
Chilimwe, ndipatse munda.
-Munthu akafuna kuti adzapeze zabwino m’tsogolo amafunika
kukonzekera.
Chiloli chinapha ngondo.
-Ukakhala munthu wachidwi ndi wofuna kudziwa chilichonse,
tsiku lina umadzakhala mboni pa mlandu woopsa, mwina
n’kupeza mavuto.
Chilosi chidabwerera lunguzi.
-Mukanyoza munthu osam’patsa moni chifukwa choti ndi mlen-
do, tsiku lina mumadzakam’peza kwawo n’kuchita manyazi.
Chilungamo chiziyenda ngati madzi.
-Chilungamo chimafunika chioneke. Tikamachita zinthu zonse,
tiyenera kumaonetsetsa kuti tikuchita zinthu mwachilungamo
kwa aliyense mosatengera maonekedwe.
Chilungamo n’chipongwe.
-Nthawi zina anthu amadana ndi kumva chilungamo chifukwa
chimamveka ngati chipongwe.
Chim’mawa chidalambalalitsa fulu bowa.
-Tizichita zinthu mofatsira ndi mwaluso osati mongofulumira,
38