Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 38
Miyambi ya Patsokwe
mavuto a mnzako.
Chili kwa mnzako ndiye “psinyitsa,” chili kwa iwe ndiye,
“psinya bwino.”
-Mnzathu akalakwa ndiye timafuna kuti alandire chilango
chowawa, koma zikakhala kwa ife, timafuna kuti atimvere chi-
soni potipatsa chilango chofewa.
Chili kwa mnzako umati “chigwire nyanga!”
-Munthu amaona vuto la mnzake ngati si vuto ayi, koma vuto
ngati lomwelo likamuonekera m’pamene amaliwona kuti ndi
phiri.
Chili kwa mnzako, utenga madzi numwera.
-Mavuto akakhala kwa ena kumakhala kosavuta kuwalangiza
zomwe anachita kuti apeze mavutowo, koma zikatigwera sititha
kumvetsa chomwe chachititsa mavutowo.
Chili kwa nyani, pusi sachitengera malonda.
-Nthawi zambiri pakati pa abale sipakhala kugulitsana zinthu
koma kungopatsana basi.
Chili n’kudza chisonkha moto paphale, chipala (phulusa) chi-
taya kuthengo.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamanena kuti alipo wina
womuposa amene akubwera.
Chilichonse chili ndi nthawi yake.
-Ndi bwino kumachita zinthu pa nthawi yake. Kumadziwa
nthawi yabwino yochita chilichonse monga kuyankhula kapena
kukhala chete.
Chilichonse chotentha, pamapeto pake chimazizira.
-Munthu wina atatopa kulumidwa ndi Nsikidzi, anaganiza
zotereka madzi kuti azikhaulitse. Kenako anatenga bulangete
37