Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 37
Miyambi ya Patsokwe
kugwira ntchito inayake, tsiku lina pamadzakhala china chotik-
umbutsa chomwe tinaiwala. Nthawi zina mavuto amatichititsa
kugwira ntchito molimbika komanso kugwira ntchito zomwe
tinkaziona ngati zopanda pake.
Chikuni cha m’bwalo chikoma n’kugwirizana.
-Kuthandizana n’kofunika kwambiri m’malo momadzipatula.
Chikuni cha utsi timafumula.
-Pakakhala munthu wosokoneza pamudzi kapena pantchito pa-
mafunika kumulangiratu kuopa kuti angasocheretse ena.
Chikuni chimodzi sichipsetsa mphika.
-Kuti ntchito iyende pamafunika kuthandizana.
Chikuni pakutha, chimataya therere.
-Nthawi zambiri ntchito imaonongeka kumapeto. Ndi bwino
kumasamala pogwira ntchito mpaka kumapeto.
Chilekwa (wamasiye) n’chosakhala kupatira chabwino.
-Nthawi zina mwana wamasiye amatha kupeza msanga
chithandizo. Zinthu zonyozeka zingathe kutipatsa zabwino.
Chilendo ndi kulumpha chiunda.
-Munthu ukangotuluka m’nyumba mwako kwina konse uma-
khala mlendo.
Chili kumunda n’chambewu, chakumudzi n’chakudya.
-Tizisunga zina kuti tidzagwiritse ntchito m’tsogolo.
Chili kumwamba ndi chamwini.
-Si bwino kukhumbira zinthu za eni kapena zinthu zomwe
tikudziwa kuti sitingathe kuzipeza.
Chili kwa mnzako n’kumati, “chigwire nyanga.”
-Sizivuta kupeza zolakwa za mnzako n’kusiya zako kapena kuu-
za ena zoti achite koma zoti iweyo sungakwanitse. Osamaderera
36